CCAP Nkhoma Synod yakana mapemphero omwe anachitika kwa a Mutharika

Advertisement
Mutharika

…Synod ikufufuza abusa ake…

Synod ya Nkhoma ya mpingo wa Church of Central Africa Presbyterian (CCAP), yati mwa abusa onse 53 omwe anapita kunyumba ya mtsogoleri wakale Peter Mutharika, m’boma la Mangochi kukachita mapemphero, abusa okwana asanu ndi awiri (7) ndi omwe synod-yi ikuwadziwa.

Malinga ndi kalata yomwe Nkhoma Synod yatulutsa yomwe watsimikiza mlembi wa zonse m’busa Vasco Kachipapa, ati abusawa analakwitsa kugwiritsa ntchito dzina la “Nkhoma Synod” pamene anapita monga a mu guru la azibusa osiyanasiya lomwe analowa (pastors fraternal).

A Kachipapa ati mwa abusa asanu ndi awiriwa (7), asanu ndi omwe akutumikira mu Synod-yi ndipo amodzi adapuma pa ubusa pamene abusa a Kawanga adachotsedwa pa ubusa mchaka cha 2020.

Kalatayi yati abusawa aphwanya ndondomeko zina za Synod yi pogwiritsa ntchito dzina la Nkhoma Synod” kufuna kupeza zokhumba zawo pa ndale ndipo achenjeza abusa ena onse kupewa kugwiritsa ntchito dzina la Nkhoma Synod” kupeza zokhumba zawo.

Kalatayi yati abusa ake omwe akutumikira omwe anapita kukapemphera ku nyumba ya PAGE ndi a Chifunilo Damalankhunda, Jacob Kadzakumanja, Stafford Makuta, Sydney Phula Banda, Sitiyoni Mtama komanso abusa a Waison Chiwaula omwe adapuma pa ubusa.

“Adindo akuyitsata bwino nkhaniyi ndipo chotsatira choyenelera chitengedwa mosakhalitsa” (the leadership is following up on the matter and an appropriate Action will be taken accordingly” inatelo kalata.

Mtsogoleri wa abusa omwe anapita Ku PAGE a Chifunilo Damalankhunda anati abusa ena anakanika kukhala nawo chifukwa cha mantha.

Iwo anati mzosabisa kuti posachedwapa akhonzano kusumilidwa.

Mtsogoleri wakale Peter Mutharika anati mzodabwitsa kuti ena sakumakondwa ndi mapemphero omwe akumachitika kunyumba kwawo ponena kuti atumiki amulundi ndi atsogoleri a ndale akuyenera kugwilira ntchito limodzi kukweza umoyo wa anthu kuthupi ndi Ku uzimu.

Posachedwapa abusa ena a mpingo omwewu wa CCAP mu Synod ya Blantyre anasumilidwa ndi komiti yosungitsa mwambo kukayankha pa chifukwa chimene anapitira kunyumba kwa a Mutharika kukachita mapemphero mu dzina la Synod-yi komanso kugwiritsa ntchito mawu oti DPP woyee!!! .

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.